Ndinazindikira kuti Moyo ndi Wamtengo Wapatali
Ndinazindikira kuti Moyo ndi Wamtengo Wapatali
UNALI M’MAWA, PA 16 APRIL, 2007. Ndinanjuta n’kubisala pakona m’chipinda china cha nyumba yosanja yotchedwa Norris Hall pa yunivesite ya Virginia Tech (Virginia Polytechnic Institute and State University). Zimene zinachitika patsikuli zinandikumbutsa kuti tiyeneradi kuyamikira Mulungu kwambiri tsiku lililonse limene tili ndi moyo.
Ndinali mu ofesi yanga ndipo ndinkafuna kupita m’maofesi a pansi kukatenga makalata anga. Kenako pulofesa wina anabwera kudzandipempha kuti ndikamukonzere kompyuta ku ofesi yake. Tikulowa mu ofesiyo, tinangomva kulira kwa mfuti m’maofesi a pansi aja. Posadziwa kuti chikuchitika n’chiyani, tinadzitsekera mu ofesiyo msangamsanga tili ndi mantha aakulu ndipo sitimadziwa kuti tiona zotani. Ndinabisala pakona n’kuyamba kupemphera kwa Yehova Mulungu mochokera pansi pamtima kuti andithandize pa chilichonse chimene chichitike.
Panthawiyi ndinakumbukira zimene zinandichitikiranso zaka 15 zapitazo ndili makaniko. Mnzanga wina ananyamula kachitini kenakake ka petulo ndipo petuloyo anangoyaka mwadzidzidzi. Pochita mantha, iyeyo anangozindikira kuti mwangozi wandiponyera kachitiniko kumaso. Mpweya wotentha unandilowa m’mapapo komanso ndinapsa kwambiri kumtunda konseku moti ananditengera kuchipatala pandege. Kuchipatalako anandiika ku malo a matenda a kayakaya kwa miyezi itatu ndipo ndinabwerera ku nyumba patatha miyezi isanu. Ndinathokoza kwambiri Mulungu kuti anandisunga n’kukhalabe ndi moyo. Zimenezi zinandiphunzitsa kuti ndiyenera kumaona kuti tsiku lililonse pa moyo wanga ndi lamtengo wapatali kwambiri. Popeza ndine wa Mboni za Yehova, zimenezi zinandithandizanso kukhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu amene anandipatsa moyo.—Salmo 90:12; Yesaya 43:10.
Ndinavulala kwambiri moti sindikanatha kupitiriza ntchito ya umakaniko. Choncho ndinaphunzira kukonza makompyuta n’kupeza ntchito ku yunivesite ya Virginia Tech. N’chifukwa chake ndinapezeka m’nyumba ya Norris Hall patsikuli.
Zipolopolo zinapitirirabe kumveka, koma sitimadziwa kuti zimene zinali kuchitika pansi pa nyumbayi zinali zoti sizinachitikepo m’mbiri yonse ya dziko la United States. Kenako munthu amene ankawomba mfutiyo anadziwombera ndipo apa n’kuti atapha anthu 32. Zonsezi zinachitika kwa mphindi 20 ndipo kenaka tinamva apolisi akulowa m’nyumbayo. Tinawaitana kuti atithandize ndipo anatitulutsa m’nyumbayo bwinobwino.
Zoopsa zimene ndinaonazi zinandiphunzitsa kuti n’zoonadi kuti chakudza sichiyimba ng’oma chifukwa sitidziwa kuti n’chiyani chitichitikire. (Yakobe 4:14) Motero m’pofunikadi kuti tizidalira kwambiri Yehova Mulungu, yemwe ndi Wopatsa moyo, ndiponso kuti tsiku lililonse tiziliona kuti ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa iye.—Salmo 23:4; 91:2.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
AP Photo/The Roanoke Times, Alan Kim