Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zina zimene Solomo anachita ndi chenjezo kwa ife?
Mulungu anadalitsa ndiponso kugwiritsa ntchito Mfumu Solomo. Koma kenako Solomo anayamba kuchita zinthu zosemphana ndi malangizo a Mulungu. Iye anakwatira mwana wa Farao yemwe ankalambira milungu yonyenga. Anakwatiranso akazi ena ambirimbiri ndipo kenako anakopedwa ndi akaziwo kuti ayambe kulambira milungu yonyenga. Tiyenera kupewa kuyamba pang’onong’ono mtima ndiponso zizolowezi zoipa. (Deut. 7:1-4; 17:17; 1 Maf. 11:4-8)—12/15, tsamba 10-12.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Sara anali mkazi woopa Mulungu komanso wabwino kwambiri?
Pamene Mulungu anauza Abulahamu kuti achoke ku Uri zinatanthauza kuti iye asiye achibale ake, anzake komanso moyo umene ankakhala n’kupita kumalo kumene sankadziwako. Koma Sara sanadandaule nazo ndipo ankakhulupirira kuti Mulungu amudalitsa. Iye ankalemekeza Abulahamu ndipo anasonyeza makhalidwe abwino kwambiri.—1/1, tsamba 8.
Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anauza Abulahamu kuti apereke mwana wake nsembe?
Pa nkhaniyi, m’pofunika kwambiri kukumbukira kuti Mulungu sanalole zoti Abulahamu aperekedi nsembe Isaki. Imeneyi inali njira yosonyeza mmene Mulungu adzaperekere nsembe Mwana wake Yesu ngakhale kuti zidzamupweteka kwambiri.—1/1, tsamba 23.
N’chiyani chikusonyeza kuti kuyambira nthawi ya atumwi, padziko lapansi nthawi zonse pakhala Akhristu odzozedwa enieni?
M’fanizo la Yesu lonena za “tirigu” ndi “namsongole,” “mbewu zabwino” zikutanthauza “ana a ufumu.” (Mat. 13:24-30, 38) Namsongole ndi tirigu zinayenera kukulira limodzi mpaka nthawi yokolola. Choncho ngakhale kuti sitinganene motsimikizira kuti ndi ndani omwe anali m’gulu la tirigu, nthawi zonse padzikoli pakhala anthu omwe ndi a m’gululi mpaka nthawi yathu ino.—1/15, tsamba 7.
Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzayambitse nkhondo ya Aramagedo?
Maboma a anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:3) Maboma adzaukira chipembedzo chonyenga. (Chiv. 17:15-18) Olambira oona adzaukiridwa. Kenako mapeto adzafika.—2/1, tsamba 9.
Kodi tingatani kuti tithane ndi khalidwe la kaduka?
Njira zotsatirazi zingatithandize: Kukonda abale athu, kucheza ndi anthu amene amakonda Mulungu, kuyesetsa kuchita zabwino ndiponso ‘kusangalala ndi anthu amene akusangalala.’ (Aroma 12:15)—2/15, tsamba 16-17.
Kodi ndi ndani amene amalankhula chinenero cha Chinawato ndipo akuthandizidwa bwanji?
Chinali chinenero cha mtundu wakale wa anthu otchedwa Aaziteki ndipo chimalankhulidwabe ndi anthu okwana 1,500,000 ku Mexico. A Mboni amalalikira m’Chinawato ndipo mabuku athu ena amapezeka m’chinenero chimenechi.—3/1, tsamba 13-14.
Muyenera kukumbukira mfundo ziti mukamapereka malangizo?
Muziyamba mwaimvetsa bwino nkhaniyo. Musafulumire kuyankha. Modzichepetsa gwiritsani ntchito Mawu a Mulungu. Ngati n’zotheka muzifufuza m’mabuku athu. Komanso pewani kusankhira ena zochita.—3/15, tsamba 7-9.
Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena za kumunyamulira katundu munthu waudindo mtunda wa makilomita awiri?—Mat. 5:41.
Pa nthawi imeneyo ku Isiraeli, Aroma amene ankalamulira ankakakamiza anthu kuti awathandize pa ntchito yawo. Pamene Yesu anauza omvera ake kuti azinyamulira katundu munthu waudindo mtunda wa makilomita awiri, ankawalimbikitsa kuti azigwira mosanyinyirika ntchito zimene anthu aulamuliro awauza.—4/1, tsamba 9.