Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Popeza kuti kukolola kunkayamba pamene Aisiraeli onse aamuna anali ku Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, nanga kodi ndani ankakolola barele woyamba kucha n’kupita naye kukachisi?
Chilamulo cha Mose chinalangiza Aisiraeli kuti: “Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m’malo amene iye adzasankha, katatu m’chaka; pamadyerero a mkate wopanda chotupitsa, pamadyerero a masabata, ndi pamadyerero a misasa.” (Deuteronomo 16:16) Kuyambira nthawi ya Mfumu Solomo kupita m’tsogolo, kachisi ku Yerusalemu ndiye malo amene Mulungu anasankha.
Pamadyerero atatuwa, oyamba ankachitika kuchiyambi kwa nyengo ya masika, kapena kuti nyengo yokolola. Madyererowa ankatchedwa Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, ndipo ankayamba litadutsa tsiku la Pasika la Nisani 14 ndipo ankachitika masiku 7 mpaka pa Nisani 21. Malinga ndi kalendala yawo yopatulika, kukolola koyamba kunkayamba tsiku lachiwiri la madyererowo, pa Nisani 16. Patsiku limeneli, mkulu wa ansembe ankatenga “mtolo wa zipatso zoyamba” za barele ndi ‘kuuweyula pamaso pa Yehova’ m’kachisi. (Levitiko 23:5-12) Popeza kuti nthawi imeneyi amuna onse ankakhala ku Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa, nanga ndani ankakolola mtolo umenewu wa barele?
Lamulo lakuti azipereka zipatso zoyamba kucha kwa Yehova pa Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa linaperekedwa ku mtundu wonsewo. Munthu aliyense sanafunikire kuyamba kukolola yekha ndi kupereka zipatso zoyamba kuchazo ku kachisi. Koma lamulolo linali lakuti anthu oimira mtundu wonsewo azichita zimenezo. Choncho, ntchito yodula barele wa Madyerero a Mkate Wopanda Chotupitsa iyenera kuti inkachitidwa ndi anthu angapo otumizidwa ku munda wa barele wapafupi ndi Yerusalemu. Pothirirapo ndemanga pankhani imeneyi, buku lina limati: “Barele akacha, ankamudula m’minda yapafupi ndi Yerusalemu. Apo ayi, ankamutenga ku minda yakwina kulikonse mu Isiraeli. Amuna odula bareleyo ankakhalapo atatu, aliyense ndi chikwakwa chake ndi mtanga wake.” (Encyclopaedia Judaica) Kenako ankapereka mtolo wa barelewo kwa mkulu wa ansembe, amene ankaupereka kwa Yehova.
Lamulo lopereka zipatso zoyamba kucha linapatsa Aisiraeli mwayi woyamikira Mulungu chifukwa chodalitsa dziko lawo ndi zokolola zawo. (Deuteronomo 8:6-10) Koma chofunika kwambiri n’chakuti mwambo wopereka nsembewu unali ‘mthunzi wa zinthu zabwino zimene zinali kubwera.’ (Aheberi 10:1) N’zochititsa chidwi kudziwa kuti Yesu Khristu anaukitsidwa pa Nisani 16, mu 33 C.E., tsiku lomwe ankapereka zipatso zoyamba kucha kwa Yehova. Ponena za Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, kukhala chipatso choyamba cha amene akugona mu imfa. . . . Koma aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyamba, kenako ake a Khristu panthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akorinto 15:20-23) Mtolo wa zipatso zoyamba kucha umene mkulu wa ansembe ankaweyula pamaso pa Yehova unkaimira Yesu Khristu woukitsidwa, amene anali woyamba kupatsidwa moyo wosatha ataukitsidwa. Motero, Yesu anatsegula njira yomasulira anthu ku uchimo ndi imfa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
© 2003 BiblePlaces.com