Anthu Okha Ndiwo Ali ndi Khalidwe Lotere
Anthu Okha Ndiwo Ali ndi Khalidwe Lotere
Jodie amachita bizinesi yothandiza anthu kuwerengera katundu wamasiye kuti adziwe mtengo wake. Nthaŵi ina, iye ankathandiza mayi wina kuwerengera katundu wa m’nyumba ya mkulu wake amene anamwalira. Ali m’kati molongosola katunduyo, Jodie anapeza mabokosi awiri akale oikamo zipangizo zowedzera nsomba omwe anali pansi pa chumuni chakale m’nyumbamo. Ataona zimene zinali m’kati mwa limodzi mwa mabokosiwo anazunguzika mutu. Munali mipukutu ya ndalama zapepala za ma 100 dola zokwana madola 82,000! Apatu n’kuti Jodie ali yekhayekha m’chipindamo. Ndiye kodi pamenepa iyeyu ayenera kutani? Kodi angotenga bokosilo mwakachetechete kapena amudziwitse mayiyo kuti wapeza ndalama?
APA Jodie anayenera kuganiza mofatsa kuti adziwe choyenerera kuchita. Khalidwe lofuna kudziwa chimene chili choyenerera kuchitali ndi limodzi mwa makhalidwe amene amachititsa kuti anthufe tikhale osiyana ndi zinyama. Buku lakuti The World Book Encyclopedia limati: “Khalidwe limodzi lapadera kwambiri la anthufe n’lakuti timatha kukhala phee n’kumadzifunsa kuti, kodi pamenepa zoyenerera kuchita n’ziti?” Galu wanjala akapeza nthuli ya nyama patebulo sangayambe wadzifunsa kaye zoti adye kapena asadye nthuliyo. Koma poti Jodie ndi munthu, iye angathe kuganiza kaye ngati zimene akufuna kuchitazo zili zoyenerera kapena ayi. Akatenga ndalamazo, ndiye kuti waba, komabe iye akudziwa kuti n’zokayikitsa kuti angagwidwe. N’zoona kuti ndalamazo sizake, komano mayi uja sakudziwa kuti pali ndalama zoterezi. Chinanso n’chakuti Jodie akapereka ndalamazi kwa mayi uja, anthu ambiri kumene iyeyu akukhala angamuone ngati wopusa.
Kodi inuyo mukanatani mukanakhala Jodie? Yankho lanu pa funso limeneli lingadalire mfundo zimene inuyo mumatsatira zokhudza khalidwe loyenerera ndiponso losayenerera.
Kudziwa Khalidwe Loyenerera ndi Losayenerera
Kwa nthawi yaitali, zipembedzo ndizo zakhala zikuuza anthu khalidwe loyenerera ndiponso losayenerera. Pankhaniyi, anthu ambiri a m’zigawo zosiyanasiyana za padziko lonse akhala akutsatira zimene limanena Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Komabe padziko pano pali anthu ambiri amene ayamba kuona kuti mfundo zosiyanasiyana zachipembedzo n’zosathandiza ndiponso kuti mfundo za m’Baibulo zokhudza khalidwe loyenerera ndi losayenerera n’zachikale. Nangano kodi anthuwa ayamba kutsatira mfundo zotani? Buku lakuti Ethics in Business Life limati “anthu asiya kumvera mfundo zachipembedzo n’kuyamba kutsatira nzeru za anthu. . . . ” Inde, anthu ambiri satsatiranso mfundo zachipembedzo, m’malo mwake amamvera akatswiri a maphunziro a khalidwe loyenerera ndi losayenerera. Paul McNeill, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro a khalidwe loyenerera ndi losayenerera komanso wa zamalamulo anati: “Ineyo ndimaona kuti akatswiri a maphunziro a khalidwe loyenerera ndi losayenerera ndiwo alowa m’malo mwa abusa . . . . Masiku ano anthu akamaganizira zochita, saganiziranso za chipembezo ayi, koma amangoganizira za khalidwe loyenerera kwa iwowo basi.”
Kodi inuyo mukathedwa nzeru, mumatani kuti mudziwe zoyenerera ndi zosayenerera kuchita? Kodi pankhani ya zoyenerera ndi zosayenerera kuchita inuyo mumatsatira mfundo za Mulungu kapena mfundo zanuzanu?