Kodi Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?
Imfa imakhudza aliyense. Koma kodi imfa ndi mathero a zonse? Kodi anthu amene anamwalira ndiye kuti basi anaiwalidwa? Kodi pali chiyembekezo chilichonse chokhudza anthu amene anamwalira?
TAONANI ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
ANTHU AMENE ANAMWALIRA SANAIWALIDWE
“Onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
Mulungu sanaiwale anthu amene anamwalira ndipo adzaukitsa onse amene ali m’manda achikumbutso.
AKUFA ADZAUKITSIDWA PADZIKOLI
“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.
Anthu mamiliyoni ambirimbiri adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kwamuyaya m’dziko la mtendere.
CHIYEMBEKEZO CHOTI AKUFA ADZAUKITSIDWA N’CHODALIRIKA
“[Mulungu] amawerenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazitchula mayina ake.”—Salimo 147:4.
Ngati Mulungu amakwanitsa kutchula nyenyezi iliyonse dzina, ndiye kuti akukumbukira anthu amene akufuna kudzawaukitsa.