“Zinthu Zakale . . . Sizidzabweranso Mumtima”
“Zinthu Zakale . . . Sizidzabweranso Mumtima”
Mlengi wathu anatiuza zimene achite posachedwapa. Iye anati:
“Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—YESAYA 65:17.
Kodi ndi ‘zinthu zakale ziti zimene sizidzabweranso mumtima’? Nkhani yonse ya m’chaputalachi ikusonyeza kuti zinthu zimenezi ndi monga kupanda chilungamo, matenda, komanso zinthu zimene zimavutitsa anthu. Kodi mavuto amenewa adzatha bwanji? Zidzatha Mulungu akadzakhazikitsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”
Tanthauzo la mawu amenewa komanso kufunika kwake zidzafotokozedwa m’nkhani yakuti: “Zinthu Zakale . . . Sizidzabweranso Mumtima.” Nkhani imeneyi idzakambidwa pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti, ‘Tetezani Mtima Wanu.’ Misonkhanoyi idzachitika kuyambira mwezi wa May ku United States ndipo kenako idzachitika m’madera osiyanasiyana padziko lonse.
Tikukupemphani kuti mudzafike kumsonkhano womwe udzachitikire kufupi ndi kwanu. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani Mboni za Yehova za kwanuko kapena lemberani kalata ofalitsa a magazini ino. Mukhoza kudziwa za malo amene kudzachitikire msonkhanowu pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.