Mfundo 7 Zothandiza Kwambiri
Mfundo 7 Zothandiza Kwambiri
MFUNDO zotsatirazi zimapezeka m’Baibulo, lomwe ndi buku lakale kwambiri lokhala ndi mfundo zothandiza. Taonani mmene mfundo zimenezi zingakuthandizireni kugwiritsa ntchito ndalama zanu mwanzeru.
1. “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.” (Mlaliki 5:10) Mawuwa analembedwa ndi mfumu Solomo ya ku Isiraeli. Iye sanali munthu wansanje kapena wosauka. Solomo anali munthu wolemera kwambiri. Choncho, iye analemba zinthu zimene zimachitikadi, osati zongolota. Anthu enanso olemera kwambiri masiku ano anenapo mawu ofanana ndi a mfumu Solomo amenewa.
2. “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi. Komabe, anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha.” (1 Timoteyo 6:8, 9) Mawu amenewa analembedwa ndi mtumwi Paulo, yemwe anasiya ntchito yake yapamwamba n’kukhala wotsatira wa Yesu Khristu. Mosiyana ndi atsogoleri a zipembedzo zambiri masiku ano, Paulo sankafuna ngakhale pang’ono kudyera masuku pamutu anthu amene ankawaphunzitsa kapena anzake. Iye ananena ndi mtima wonse kuti: “Sindinasirire mwa nsanje siliva, golide kapena chovala cha munthu. Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zosowa zanga ndi za amene ali nane.”—Machitidwe 20:33, 34.
Luka 14:28) Fanizo limene Yesu ananenali lingatithandize kwambiri kuti tisamawononge ndalama. Pogula zinthu pa ngongole, tiyenera kupewa kuchita zinthu mopupuluma. Tiyenera kuona ngati tikufunikiradi zinthuzo komanso ngati tili ndi ndalama zokwanira.
3. “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” (4. “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miyambo 22:7) Vuto la zachuma lomwe linachitika padziko lonse, likusonyeza kuti kugula zinthu pa ngongole n’kosathandiza. Michael Wagner analemba m’buku lake lija kuti: “Masiku ano si zachilendo kuona munthu akukhala ndi ngongole za ndalama zoposa madola 9,000, zomwe nthawi zambiri amazitenga kudzera pa makadi ogulira zinthu okwana anayi kapena kuposa.”—Your Money, Day One.
5. “Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza, koma wolungama amakomera mtima ena ndipo amapereka mphatso.” (Salimo 37:21) Anthu ena akabwereka ndalama sabweza. Koma anthu amene amaona kuti ubwenzi wawo ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri amaonetsetsa kuti abweza ngongole zawo zonse, ngati n’zotheka, komanso amakhala ndi mtima wopatsa.
6. “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.” (Salimo 37:25) Mawu amenewa analembedwa ndi Davide, yemwe anachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo pa moyo wake. Kwa zaka zambiri, iye ankakhala mothawathawa chifukwa choopa kuphedwa, moti nthawi zina ankakhala kuphanga, kapena kukabisala m’dziko lachilendo. Koma kenako anadzakhala mfumu ya Aisiraeli. Nthawi yonse imene anakhala ndi moyo, Davide anaona Mulungu akumusamalira. Choncho mawu amene ananena pamwambawa ndi oona.
7. “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mawu amenewa ananenedwa ndi Yesu Khristu. “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake,” Yesu ali padziko lapansi ankakonda kutumikira anthu ena. Panopa iye ali ndi moyo wauzimu kumwamba, kudzanja lamanja la “Mulungu wachimwemwe,” Yehova.—Aheberi 12:2; 1 Timoteyo 1:11.
Palibenso chinthu china chofunika kwambiri chimene tingachite pa moyo wathu kuposa kutsatira chitsanzo cha Yesu chochita zonse zimene tingathe kuti tithandize anthu ena. Mwina nanunso mwaona kuti ndi nzeru kusunga ndalama kuti muzithanso kuthandizira ena, kusiyana ndi kuwononga ndalamazo mwachisawawa.