Malangizo Odalirika Komanso Opereka Chiyembekezo
Malangizo Odalirika Komanso Opereka Chiyembekezo
MOSIYANA ndi ziwanda, Yehova Mulungu ndi wanzeru zonse ndiponso wamphamvu zonse. Komanso, iye ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Malangizo ake amathandiza nthawi zonse, ndipo sachita kulipiritsa. Iye amatifuniranso zabwino nthawi zonse. Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi anthu ochita zamatsenga komanso asing’anga owombeza. Mulungu amati: “Inu nonse amene mukumva ludzu [lauzimu], bwerani mudzamwe madzi. Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye. Inde bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka popanda ndalama ndiponso popanda mtengo wake. N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa? Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.”—Yesaya 55:1, 2.
Popeza kuti Baibulo linauziridwa ndi Mlengi wathu wachikondi, limatipatsa chiyembekezo, chitetezo chauzimu, cholinga chenicheni pa moyo, komanso mfundo zabwino kwambiri zoti tiziyendera. Taganizirani mofatsa mafunso otsatirawa ndi malemba ochokera m’Baibulo amene akuyankha mafunsowo.
[Bokosi patsamba 7]
● Kodi ndingapeze bwanji mtendere weniweni? Baibulo limati: “Yehova, Wokuwombolani, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.’”—Yesaya 48:17, 18.
● Kodi zinthu zoipa sizidzatha? “Owongoka mtima ndi amene adzakhale m’dziko lapansi, ndipo opanda cholakwa ndi amene adzatsalemo. Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Inde, anthu oipa, komanso angelo oipa, adzawonongedweratu, ngati kuti awonongedwa ndi moto.—Chivumbulutso 20:10, 14.
● Kodi matenda ndi mavuto zidzatha? “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo [kapena kuti mavuto ambirimbiri amene tikukumana nawo masiku ano] zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Mosiyana ndi ziwanda, Mulungu sanama. Ndipotu iye “sanganame.” (Tito 1:2) Komanso, monga momwe nkhani yomaliza pa nkhani zino ikufotokozera, choonadi chake chimamasula ndiponso chimapatsa moyo.—Yohane 8:32; 17:3.