Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Mu 1980, pafupifupi theka la anthu onse a ku Germany ankaona kuti Khirisimasi ndi mwambo wachipembedzo. Koma panopo ndi anthu 8 okha pa anthu 100 alionse amene amaona kuti ndi mwambo wachipembedzo.—TV NEWS CHANNEL N24, GERMANY.
▪ “Kwanthawi yoyamba m’mbiri ya United States, pa anthu 100 alionse, munthu mmodzi kapena kuposerapo ali kundende . . . M’dziko limeneli anthu amene ali kundende alipo pafupifupi 1.6 miliyoni.”—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.
▪ Pakafukufuku wina ku Spain anapeza kuti “pafupifupi anthu onse amene anawayeza” anali ndi mankhwala enaake m’thupi mwawo amene “anthu m’mayiko osiyanasiyana amawaona kuti angavulaze thanzi la munthu.”—UNIVERSITY OF GRANADA, SPAIN.
▪ “Malinga ndi zimene anapeza m’mayiko ena, ndalama zomwe amapeza pa misonkho ya ogulitsa fodya ndi zochuluka kwambiri kuposa zimene amawononga poletsa anthu kulima ndi kugulitsa fodya.”—WORLD HEALTH ORGANIZATION, SWITZERLAND.
▪ Chisilamu chili ndi anthu ambiri kuposa mpingo wa Katolika. Mu 2006, anthu 19 pa 100 alionse padziko lapansi anali Asilamu ndipo anthu 17 pa 100 alionse anali a mpingo wa Katolika.—REUTERS NEWS SERVICE, BRITAIN.
Makaiti Akuthandiza Sitima Zapamadzi
Masiku ano, chifukwa cha kukwera mtengo kwa mafuta komanso kudera nkhawa kwambiri zachilengedwe, anthu omwe ali ndi sitima zapamadzi akufufuza njira zothandiza kuti azigwiritsa ntchito mafuta ochepa komanso kuti asamawononge mpweya. Ndipo ayambiranso kugwiritsa ntchito mphepo poyendetsa sitima. Nyuzipepala ina (Frankfurter Allgemeine Zeitung) inanena kuti anthu ena ayamba kugwiritsa ntchito makaiti kuyendetsera sitima zapamadzi. Kaiti ikakhala m’mwamba mamita 300 imathandizira kuyendetsa sitima ndipo woyendetsa amatha kuzimitsira injini ya sitimayo. Posachedwapa kaiti inathandiza sitima ina yaikulu yonyamula katundu kuoloka nyanja yaikulu ya Atlantic. Kaitiyi inali yaikulu mamita 20 m’litali ndiponso mamita 8 m’lifupi.
Mmene Zimapulumukira Chilala
Nyuzipepala ina inati: “Panthawi ya chilala, tiana ta mtundu winawake wa ntchentche za ku Africa timasintha kukhala zinthu zolimba kwambiri kuti tipulumuke.” (Science News) Tiana ta ntchentche timeneti tikakhala kuti tilibe madzi m’thupi, tinthu tina m’thupi mwawo timasintha n’kukhala tinthu tooneka ngati magalasi tofanana ndi shuga wosungunuka akauma. Zikatere, thupi lawo limasiyiratu kupukusa chakudya ndipo timakhala “ngati takufa.” Tianati tikhoza kukhala choncho kwa zaka 17 kufikira pamene mvula idzabwere kuti tibwererenso mwakale.
Malo Abwino Kwambiri Oonerako Zakuthambo
Gulu lina la anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana aika makina oonera zakuthambo ku Dome Argus ndipo malo amenewa ali pamalo okwera mamita 4,000 kum’mawa kwa mapiri a Antarctic. Malo amenewa ndi okwera kwambiri m’derali. Chifukwa choti malowa ali pamtunda wa makilomita 1,000 kuchoka kum’mwera kwenikweni kwa dziko lapansi amakhala ozizira kwambiri ndipo nthawi zina kumakhala mdima wandiweyani. Malo amenewa amakhala ndi kamphepo kayaziyazi komanso kumatha kukhala mdima kwa miyezi inayi. Anthu amati ku Dome Argus ndi malo abwino kwambiri oonerako zakuthambo padziko lonse lapansi. Mkulu wa pamalo oonera zakuthambo amenewa wa ku China dzina lake Lifan Wang, ananena kuti, pamalo amenewa “n’zotheka kujambula zithunzi za zinthu zakuthambo zooneka bwino kwambiri komanso motchipa poyerekezera ndi kutumiza m’mlengalenga chipangizo choonera zinthu zakutali.”