Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungathe Kuthandiza Anthu Akufa?

Kodi Mungathe Kuthandiza Anthu Akufa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mungathe Kuthandiza Anthu Akufa?

“Kuyambira pachiyambi, tchalitchi chakhala . . . chikupereka mapemphero othandiza [akufa] . . . n’cholinga choti ayeretsedwe, ndiponso kuti apeze mwayi wapadera woonana ndi Mulungu.”—Amatero “Katekisima Wachikatolika.”

ANTHU amitundu yonse amafunitsitsa kudziwa za mmene akufa alili. Mwina inuyo munakhalapo ndi chisoni pamene munthu yemwe munali kum’konda anamwalira. Mwina mumafuna kudziwa kuti kaya anthu akufa amapitirizabe kudziwa zinthu, kaya akuzunzika kapena akusangalala, ndiponso ngati pali chilichonse chomwe mungachite kuti muwathandize.

Anthu ambiri opembedza amakhulupirira kuti angathe kuthandiza anthu akufa. Mwachitsanzo, Ahindu amakhulupirira kuti kutentha mitembo ya abale awo m’mphepete mwa mtsinje wa Ganges ndi kutayira phulusa lake m’madzi a mumtsinjewo, kungachititse kuti mzimu wa wakufayo ukhale mu mtendere wosatha. Ku mayiko a ku Asia, Abuda amatentha mapepala opangidwa ngati magalimoto, nyumba, zovala, ndi ndalama, n’chikhulupiriro choti womwalirayo adzagwiritsa ntchito zinthuzo kudziko lina lomwe wapita. Ku Africa kuno, anthu amathira nsembe za mowa pambali pa manda, n’cholinga choti wakufayo alandire.

Chikatolika chimaphunzitsa kuti ngati munthu wamwalira asanalape ena mwa “machimo aakulu,” ndiye kuti wadzichotsa yekha m’chiyanjo cha Mulungu. Zikatere ndiye kuti “ali ku ‘helo.’” Koma chimaphunzitsa kuti munthu amene amayanjidwa ndi Mulungu angakhale ndi chiyembekezo chodzalandira “chimwemwe chachikulu” kumwamba pamodzi ndi Mulungu, komano asanalandire madalitso amenewa, ayenera kuyeretsedwa kaye kuti akhale wangwiro. Kuti ayeretsedwe angafunike kupita ku purigatoriyo komwe amakapirira “moto woyeretsa” monga chilango cha machimo ake omwe angakhululukidwe. Komabe, munthu yemwe ali ku purigatoriyo, angathandizidwe ndi mapemphero omufunira zabwino ndiponso Misa zochitikira m’tchalitchi. Anzake ndi achibale a munthu wakufayo nthawi zambiri amalipirira mapemphero oterowo.

N’kwachibadwa kufuna kuchita zonse zomwe tingathe pofuna kuthetsa mavuto amene achibale athu angakumane nawo. Ngati kuwathandiza n’kothekadi, kodi Mulungu sakanafotokoza bwinobwino mmene tingawathandizire? Tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza kuthandiza akufa.

Mmene Akufa Alili

Miyambo yonse yomwe takambiranayi yagona pa chikhulupiriro choti mzimu sumafa, kapena kuti mbali ina ya munthu imapitirizabe kukhala ndi moyo thupi lake likafa. Kodi zimenezi n’zimene Baibulo limaphunzitsa? “Amoyo adziwa kuti tidzafa,” limatero Baibulo, “koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika. Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kali konse kachitidwa pansi pano. Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 6, 10.

Ponena za mmene anthu akufa alili, wamasalmo analemba kuti: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:4.

Mawu a m’Baibulo ndi odalirika ndiponso omveka. Kodi inuyo mukuganiza kuti bambo wachikondi angazunze ana ake chifukwa chakuti anawo ali ndi uchimo wochita kubadwa nawo? (Genesis 8:21) Mwachidziwikire, sangatero. Nangano Atate wathu wakumwamba angachite bwanji zimenezi? Pamene anthu ena mu Israyeli wakale anayamba kutsanzira miyambo yachikunja yopereka nsembe kwa milungu yonyenga mwa kuotcha ana awo, Yehova anadzudzula khalidwe loipalo, ndipo anati zimenezo ndi zinthu zimene ‘sanauze iwo, sizinalowe m’mtima mwake.’—Yeremiya 7:31.

Uchimo umabweretsa imfa, osati kuzunzika pambuyo pamoyo uno. Mogwirizana ndi Malemba, “mphotho yake ya uchimo ndi imfa,” ndipo “iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.”—Aroma 5:12; 6:7, 23.

Anthu akufa sakuzunzika. M’malo mwake, ali ngati akugona tulo tatikulu, ndipo sangathe kudziwa kapena kuganiza chilichonse, chabwino kapena choipa. Choncho, sitingachitenso kufunsa kuti zonse zomwe anthu amachita poyesayesa kuthandiza anthu akufa n’zosagwirizana ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa.

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani cha Akufa?

Zimenezi sizikutanthauza kuti abale anu okondedwa omwe anamwalira adzakhala osadziwa kanthu mpaka kalekale. M’malo mwake, ali ndi chiyembekezo chabwino.

Asanaukitse bwenzi lake Lazaro, Yesu anati akupita “kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Panthawi inanso, Yesu anati “onse ali m’manda [“a chikumbutso,” NW] adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Anthu oukitsidwawo adzakhala atamasulidwa ku machimo amene anawachita m’moyo wawo wakale ndipo sadzafunikiranso kuzunzidwa chifukwa cha zomwe anachitazo. Iwo adzakhala ndi mwayi wophunzira momwe angasangalalire ndi moyo m’dziko labwino kwambiri. Chiyembekezo chimenechi n’chabwino kwambiri!

Ngati chiyembekezochi chikukusangalatsani, musazengereze kutsimikizira kudalirika kwa malonjezo amenewa. Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi akufa amadziwa kanthu?—Salmo 146:4; Mlaliki 9:5, 6, 10.

▪ Kodi Mulungu angalole kuti anthu akufa azivutika kumoto?—Yeremiya 7:31.

▪ Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa akufa?—Yohane 5:28, 29.