Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Chaka chatha chinali chotentha kwambiri kumpoto kwa dziko lapansi kuyambira pamene anayamba kulemba zimenezi” ndi “chachiwiri kutentha kwambiri padziko lonse lapansi.” “Zaka eyiti pa zaka 10 zotentha kwambiri [kuyambira pamene anayamba kulemba zimenezi] zinapezeka pa zaka 10 zapitazi.”—BBC NEWS, BRITAIN.

Nyengo ya mphepo za mkuntho ku madera ozungulira nyanja ya Atlantic ya chaka cha 2005 inali “ndi mphepo zamkuntho zambiri” ndiponso “tingati . . . inali yowononga kwambiri” chiyambireni kulemba zimenezi. Mphepo za mkuntho 7 pa mphepo za mkuntho 14 zimene zinachitika zinali zothamanga makilomita oposa 177 pa ola limodzi.—U.S. NATIONAL OCEANIC AND ATMOSPHERIC ADMINISTRATION.

“Mu 1850, ku Glacier National Park ku Montana [ku United States] kunali mathanthwe a madzi oundana okwana 150. Tsopano alipo 27.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.

“Zoona zake pa nkhani ya mfundo za maboma osiyanasiyana zolimbana ndi kusintha kwa nyengo, n’zoti palibe dziko limene lidzafune kuwononga ndalama zake kuti lithane ndi vuto limeneli.”—TONY BLAIR, NDUNA YAIKULU YA KU BRITAIN.

Kodi Akatolika Akulalikira “ku Nyumba ndi Nyumba”?

Malinga ndi zimene ananena Cláudio Hummes, bishopu wamkulu wa mumzinda wa São Paulo, chiwerengero cha anthu a ku Brazil omwe ali Akatolika chatsika kuchoka pa anthu 83 pa anthu 100 alionse kufika pa anthu 67 pa anthu 100 alionse pa zaka 14 zapitazi. Bishopu wamkuluyu anati chomwe chachititsa zimenezi n’chifukwa chakuti tchalitchi “pa zifukwa zosiyanasiyana, chikulephera kulalikira mokwanira uthenga wabwino kwa mamembala ake obatizidwa.” Hummes anati: “Tiyenera kuwafika pamtima Akristu athu, ku nyumba ndi nyumba, m’masukulu, m’zipatala, m’mayunivesite, ndi m’malo ena otero, osati m’matchalitchi mokha.” Nyuzipepala ya pa Intaneti yotchedwa Folha Online inati ntchito imeneyi iyenera kugwiridwa ndi anthu wamba omwe aphunzitsidwa kukhala amishonale. Kuperewera kwa ansembe ndi vuto limodzi lalikulu lomwe tchalitchi cha Katolika chikukumana nalo ku Brazil ndi mayiko ena onse a ku Latin America.

Kuvomerezedwa Mwalamulo ku Germany

Pa chigamulo chimene chinafalitsidwa pa February 10, 2006, khoti lalikulu ku Leipzig, ku Germany, linagamula kuti Boma la Berlin liyenera kuona bungwe la Mboni za Yehova ku Germany lotchedwa Religious Association of Jehovah’s Witnesses, monga bungwe lomwe si lamalonda lovomerezeka ndi boma. Amenewa anali mapeto a mlandu womwe watenga zaka 15. Panthawi imeneyi, mlanduwu unazengedwa ndi makhoti osiyanasiyana a ku Germany, kuphatikizapo khoti lapamwamba. Monga bungwe lomwe si lamalonda, bungwe la Mboni za Yehova ku Germany la Religious Association of Jehovah’s Witnesses lili ndi ufulu wosalipira msonkho ndiponso lili ndi maufulu ena amene zipembedzo zina zikuluzikulu m’dzikolo zili nawo.

Achinyamata a ku China Akodwa ndi Masewera a pa Intaneti

Nyuzipepala ya ku Hong Kong yotchedwa South China Morning Post inati “achinyamata ambiri a ku China akodwa kwambiri ndi masewera a pa Intaneti.” Vutoli likuonekanso pakati pa achinyamata a ku mayiko ena a ku Asia, monga ku Hong Kong, ku Japan, ndi ku Republic of Korea. Nyuzipepalayo inati: “Kuwonjezeka kwa mtima wofuna kupita pa Intaneti n’kuiwala zonse zomwe zikuchitika kunjaku kukusonyeza zotsatirapo zoipa zimene zabwera chifukwa choti makolo amayembekezera ana awo kukwanitsa zinthu zovuta kwambiri ndiponso chifukwa cha mpikisano waukulu umene umakhalapo kuti wachinyamata atengedwe ku yunivesite.” Akuti mwina achinyamata okwana sikisi miliyoni a ku China akufunika kuthandizidwa kuwonjoka mu msampha umenewu.