Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Chaka chilichonse ana pafupifupi sikisi miliyoni—mmodzi m’masekondi asanu alionse—amafa chifukwa cha kudya moperewera.”—JAMES T. MORRIS, MKULU WA BUNGWE LA WORLD FOOD PROGRAMME
▪ Chiwerengero chotulutsidwa ndi boma cha anthu omwe anafa ndi mphepo ya mkuntho ya Katrina, yomwe inawomba kum’mwera kwa dziko la United States mu August 2005, chaposa 1,300.—THE WASHINGTON POST, U.S.A.
▪ Chivomezi chomwe chinagunda kumpoto kwa mayiko a Pakistan ndi India mu October 2005, chinapha anthu oposa 74,000.—BBC NEWS, BRITAIN.
▪ Lipoti lina linanena kuti “padziko lonse, anthu pafupifupi 1,200,000 amafa pangozi za pamsewu chaka ndi chaka.”—SOUTH AFRICAN MEDICAL JOURNAL, SOUTH AFRICA.
Chuma Chovuta Kusunga
Akuluakulu a Tchalitchi cha Roma Katolika athedwa nzeru pankhani ya mmene angatetezere ziboliboli ndi zojambulajambula zokongoletsera matchalitchi a ku Peru, za m’nthawi yomwe dzikolo linkalamulidwa ndi dziko la Spain. M’zaka zisanu ndi chimodzi zapitazi, matchalitchi 200 akhala akulimbana ndi mbava. M’zaka 15 zapitazi, mu mzinda umodzi wokha, wa Cuzco, munabedwa ziboliboli ndi zojambulajambula pafupifupi 5,000, ndipo zambiri mwa zinthu zimenezi ndi zithunzi za penti wa oilo. Palibe amene akudziwa bwinobwino kuti ndi zinthu zingati zimene zabedwa m’dziko lonselo. Pofuna kuteteza chumachi kuti chisabedwe, matchalitchi ena amakachibisa, koma sabisa m’malo abwino. Zina mwa zithunzi za penti wa oilo za pa parishi ina zinadyedwa ndi makoswe.
Odziwa Ntchito Zamanja Akusowa ku Finland
Mafakitale ndi makampani a ntchito zamanja m’dziko la Finland akusoweratu anthu odziwa ntchito zamanja amene amaliza maphunziro awo oyamba, monga akalipentala, okonza mapaipi a madzi, owotcherera zinthu, omanga nyumba, amakaniki, oyendetsa makina m’mafakitale, ndi manesi. Chifukwa? Nyuzipepala ya Helsingin Sanomat inanena kuti maganizo a anthu ambiri ali popita ku yunivesite. Heikki Ropponen, wa ku bungwe la Federation of Finnish Retailers, anati: “N’kupanda nzeru kuphunzitsa mbadwo wonse maphunziro aukachenjede monga udokotala ndi za sayansi. Tikufunika kuona kuti maphunziro a ntchito zamanja ndi ofunika kwambiri.”
Mlandu Uwakomera ku France
Pa December 1, 2005, khoti la apilo ku Paris, m’dziko la France, linalamula nduna ya za m’dziko kumeneko kuti ilole Mboni za Yehova kuona zikalata za apolisi zomwe anagwiritsa ntchito mu 1996 poika Mboni pamndandanda wa timagulu tampatuko. Mndandandawo unakonzedwa mwam’tseri, ndipo ankausunga mwachinsinsi, n’kumanena kuti akutero pofuna ‘kuteteza boma ndi anthu.’ Koma khotilo linapeza kuti ‘mfundo zomwe zinatchulidwa m’zikalatazo, za mmene ntchito ya Mboni imakhudzira ena, sizinali zokwanira.’ Ngakhale kuti zinali choncho, mndandandawo wakhala ukugwiritsidwa ntchito mobwerezabwereza poikira kumbuyo anthu amene amachitira nkhanza Mboni za Yehova ku France.
“Ntchito Yaikulu Yodzala Mitengo”
Kudyetsa ziweto pamalo amodzimodzi kwa nthawi yaitali, kusowa kwa mvula, kudula mitengo mwachisawawa, ndi kuwononga zinthu za m’madzi mopitirira muyeso, kwachititsa kuti madera akuluakulu a ku China akhale zipululu. Motero, akuluakulu a dziko la China anayamba “ntchito yaikulu kwambiri yobwezeretsa zachilengedwe,” inatero magazini ya New Scientist. “Pantchito imeneyi, yomwe ikutchedwa ‘ntchito yaikulu yodzala mitengo,’ adzala mitengo yambiri pofuna kutsekereza fumbi kuti lisamafike m’maderawa.” Akudzalanso udzu ndi zitsamba n’cholinga choti dothi lisamauluzike. Ntchitoyi, yomwe inayamba mu 1978 ndipo cholinga chake ndi choti maekala 86 miliyoni akhale ndi mitengo ndi zomera zimene zimapirira chilala, tsopano ili m’katikati.