Kodi Kukonda Chuma N’kutani Makamaka?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Kukonda Chuma N’kutani Makamaka?
ANTHU amabadwa ali ndi mtima wofuna kuchita zinthu zauzimu ndiponso wofuna kulambira Mulungu. Komabe popeza anthu analengedwa kuchokera kuzinthu za padziko, amafuna kukhala ndi zinthu zotero ndipo amasangalala kukhala ndi chuma. Akristu ena ali ndi chuma chochuluka kwambiri. Kodi pamenepa ndiye kuti oterowo ndi anthu okonda chuma komanso anthu osakonda kwenikweni zinthu zauzimu? Kapena kodi tinene kuti osauka sangakhale anthu okonda chuma koma okonda kwambiri zinthu zauzimu?
Ndithu mukhoza kuvomereza kuti kukonda chuma si kungokhala ndi chuma kapena katundu wambiri ayi. Taonani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kukonda chuma ndiponso zosonyeza mmene tingapeŵere zoopsa zimene chuma chimabweretsa pamoyo wauzimu.
Anali Achuma Komanso Aulemerero
Ena mwa atumiki a Mulungu okhulupirika a m’Baibulo anali achuma komanso aulemerero wawo. Mwachitsanzo, Abrahamu “anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndi siliva ndi golidi.” (Genesis 13:2) Yobu ankadziŵika kuti “anaposa anthu onse a kum’maŵa” chifukwa chakuti anali ndi zoŵeta ndiponso antchito ambiri. (Yobu 1:3) Mafumu a Israyeli, monga Davide ndi Solomo anali ndi chuma chambiri kwabasi.—1 Mbiri 29:1-5; 2 Mbiri 1:11, 12; Mlaliki 2:4-9.
M’mipingo ya m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino munali Akristu ena achuma. (1 Timoteo 6:17) Akuti Lidiya anali ‘wogulitsa chibakuwa, wa kumudzi wa Tiyatira, amene ankapembedza Mulungu.’ (Machitidwe 16:14) Nthaŵi imeneyo nsalu zachibakuwa zinali zokwera mtengo kwambiri ndipo kaŵirikaŵiri zinkapezeka ndi anthu apamwamba kapena achuma. Choncho n’kutheka kuti Lidiya anali wachuma ndithu.
Komanso m’Baibulo muli anthu ena osauka kwambiri amene ankalambira Yehova mokhulupirika. Mabanja ena anasauka chifukwa cha masoka achilengedwe, ngozi, ndiponso kuferedwa. (Mlaliki 9:11, 12) Ziyeneratu kuti zinali zopweteka kwambiri kwa anthu osaukawo kumaona anzawo akusangalala ndi chuma chawo kapena katundu amene anali naye! Ngakhale zinali choncho, kukanakhala kulakwa kuti iwowo azinena achumawo kuti ndi anthu okonda chuma kapenanso kunena kuti osaukawo ndiwo amene ankatumikiradi Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Taonani chimene makamaka chimapangitsa kuti munthu akhale wokonda chuma.
Kukonda Ndalama
Buku lina lotanthauzira mawu limati kukonda chuma ndiko “kumangoganizira kwambiri za chuma mmalo moganizira za nzeru kapena zinthu zauzimu.” Choncho kukonda chuma kumachokera
pa zinthu zimene timaziganizira kwambiri, zimene timazifuna kuposa china chilichonse, ndiponso zimene sitigona nazo tulo. Zimenezi n’zimene zili m’zitsanzo ziŵiri za m’Baibulo izi.Yehova anadzudzula kwambiri Baruki, yemwe anali mlembi wa mneneri Yeremiya. Zikuoneka kuti Baruki anali wosauka chifukwa cha mmene zinthu zinalili ku Yerusalemu panthaŵiyo komanso chifukwa chogwirizana kwambiri ndi Yeremiya, yemwe anali munthu wodedwa. Ngakhale zinali choncho, Yehova anamuuza kuti: “Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune.” N’kutheka kuti Baruki anayamba kukhala ndi mtima wokonda chuma, n’kuyamba kumangoganizira za chuma kapena kulemera kwa anthu enaake. Yehova anakumbukutsa Baruki zakuti Iye adzam’pulumutsa pa chiwonongeko cha Yerusalemu koma katundu wake sadzapulumuka.—Yeremiya 45:4, 5.
Yesu anasimba fanizo la munthu amenenso ankangoganizira za chuma. Munthu ameneyu ankangoganizira za chuma chake mmalo moti agwiritsire ntchito chuma chakecho potumikira Mulungu m’njira zina. Munthu wachumayu anati: “Ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, . . . ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.” Kenaka Yesu anati: “Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.”—Luka 12:16-21.
Kodi pa nkhani ziŵirizi mfundo yake njotani kwenikweni? Nkhanizi zikutithandiza kuona kuti munthu amakhala wokonda chuma, osati chifukwa cha zinthu zimene ali nazo, koma chifukwa cha kuona zinthuzo ngati ndizo zofunika kwambiri kuposa china chilichonse. Mtumwi Paulo anati: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasokera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Mavuto amakhalapo chifukwa chofunitsitsa kukhala wachuma ndiponso kukonda kwambiri zimene tili nazo.
M’pofunika Kumadziona Bwino
Kaya akhale achuma kapena ayi, Akristu amakhala osamala kuti apeŵe msampha wa kukonda chuma. Chuma chimanyengeza ndipo chikhoza kumulepheretsa munthu kukonda zauzimu. (Mateyu 13:22) Tingathe kusiya kukonda zinthu zauzimu mosadziŵa n’kuyamba kukonda chuma ndipo mapeto ake tingakumane ndi zinthu zoopsa kwabasi.—Miyambo 28:20; Mlaliki 5:10.
Choncho, Akristu ayenera kuona bwino kuti ndi zinthu zotani zimene amazikonda kwambiri m’moyo wawo. Kaya ali ndi chuma chochepa kapena chochuluka, anthu amene amaganizira kwambiri zauzimu amafunitsitsa kumvera mawu a Paulo akuti asayembekezere “chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.”—1 Timoteo 6:17-19.