Kodi Kuyenda Pandege N’kwabwinobe?
Kodi Kuyenda Pandege N’kwabwinobe?
ZIGAŴENGA zalanda ndege zinayi zonyamula anthu. Kenaka ndegezo zikuchita ngozi. Zawomba nyumba zodziŵika bwino. Zithunzi za ndege yaikulu ikugunda nyumba ina yosanja akuzionetsa kambirimbiri pa TV.
Inde, chiwembu cha pa September 11, 2001, chachititsa kuti tsopano anthufe tiyambe kuchita mantha kwambiri poopa zigaŵenga. Zigaŵenga zayamba kuloŵerera kundege pofuna kupha anthu, ndipo ndegezo zasanduka mabomba awo.
Motero panopa anthu ena amene poyamba sankaopa ulendo wa pandege ayamba kuchita mantha poopa chiwembu cha zigaŵenga. Ambiri chawawonjezera manthaŵa n’chakuti chiwembu cha pa September 11 chitachitika, ndege zingapo zakhala zikuchita ngozi pazokha osati chifukwa cha zigaŵenga.
N’zoona kuti anthu ambiri padziko lonse ulendo wa pandege sangaukwanitse. Koma palinso anthu ena amene nthaŵi zonse satha kuchitira mwina koma kuyenda pandege basi. Pali anthu ena amene amagwira ntchito zofunika kuyendayenda amene sangathe kupeŵa ulendo wa pandege. Komanso amishonale achikristu ndiponso Akristu ena nthaŵi zambiri amayenda ulendo wa pandege wautali akamapita ndiponso akamachokera kumene akutumikira. Nthaŵi zina ngakhale anthu osauka amayenera kuwakweza ndege basi chifukwa cha matenda a mwadzidzidzi. Oyendetsa ndege ambirimbiri ndiponso anthu ena ochita ntchito zina m’ndegemo amakhalira moyo zomwezo.
Ngakhale kuti anthu ambiri oyenda pandegeŵa mitima sikhazikika akakhala paulendo, asananyamuke amafunikanso kulimbikitsa akazi kapena amuna awo kuti asade nkhaŵa ndiponso kuuza ana awo kuti asaope. Ndipo popeza tsopano anthu akakhala paulendo wa pandege thupi limachita kuyendayenda, ena ayamba kukayikira ngati ulendo wa pandege udakali wabwinobe kuposa maulendo ena.
Pofuna kuzitsata bwino nkhani zimenezi, a magazini ya Galamukani! analankhula ndi anthu odziŵa zachitetezo, ogwira ntchito pabwalo la ndege, akuluakulu a makampani a ndege, ndiponso anthu okonza ndege. Zikuoneka kuti anthu onseŵa akugwirizana pa mfundo yakuti: Ngakhale kuti mpaka pano ulendo wa pandege ndiwo uli wabwino kwambiri, pakufunika njira zatsopano zotetezera anthu apaulendowu malinga n’kuti kwabwera zinthu zina zoopsa paulendo wotere.
Nkhani zotsatirazi zilongosola mavuto ena amene alipo ndiponso zimene inuyo mungachite panokha kuti muyende pandege mtima uli m’malo.