Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 3

Kulanditsidwa ku Igupto Mpaka pa Mfumu Yoyamba ya Israyeli

Kulanditsidwa ku Igupto Mpaka pa Mfumu Yoyamba ya Israyeli

Mose anatsogolera Aisrayeli kutuluka mu ukapolo mu Igupto kumka ku Phiri la Sinai, kumene Mulungu anawapatsa malamulo ake. Kenako, Mose anatumiza amuna 12 kukazonda dziko’lo la Kanani. Koma 10 anadza ndi mbiri yoipa. Iwo anachititsa anthu kufuna kubwerera ku Igupto. Chifukwa cha kusakhulupirira kwao, Mulungu anawalanga mwa kuchititsa Aisrayeli kupupulika-pupulika m’chipululu kwa zaka 40.

Potsiriza, Yoswa anasankhidwa kutsogoza Aisrayeli kolowa m’Kanani. Kuti awathandize kulanda dziko’lo, Yehova anachititsa zozizwitsa kuchitika. Iye anaimitsa Mtsinje wa Yordano, malinga a Yeriko kugwa, dzuwa kuima kwa tsiku lathunthu. Zitapita zaka zisanu ndi chimodzi, dziko’lo linalandidwa kwa Akanani.

Kuyambira pa Yoswa, Israyeli kwa 356 analamulidwa ndi oweruza. Timaphunzira za ambiri a iwo kuphatikizapo Baraki, Gideoni, Samsoni ndi Samueli. Timawerenga’nso za akazi onga ngati Rahabi, Debora, Yaeli, Rute, Naomi ndi Delila. Chigawo CHACHITATU chonse, chimalowetsamo zaka 396 za mbiri.