Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 98

Pa Phiri la Azitona

Pa Phiri la Azitona

UYU ndi Yesu pa Phiri la Azitona. Amuna anai ali naye’wo ndiwo atumwi ake. Iwo ndi abale Andreya ndi Petro, ndipo’nso abale’wo Yakobo ndi Yohane. Uyo mukumuona cha uko’yo ndi kachisi wa Mulungu mu Yerusalemu.

Papita masiku awiri chiyambire pamene anakwera bulu kulowa mu Yerusalemu. N’Lachiwiri. M’mawa wa tsiku’lo Yesu anali pa kachisi. Pamenepo ansembe anayesa kugwira Yesu kuti amuphe. Koma iwo anali kuopa kuchita izi chifukwa anthu anakonda Yesu.

‘Njoka inu ndi ana a njoka!’ anawatero Yesu atsogoleri achipembedzo. Ndiyeno iye anati Mulungu akawalanga chifukwa cha zoipa zonse zimene iwo anachita. Pambuyo pake Yesu anadza ku Phiri la Azitona, ndipo atumwi anai’wa anayamba kufunsa mafunso. Kodi mukudziwa zimene iwo akufunsa Yesu?

Atumwi’wo akufunsa zinthu zina za m’tsogolo. Iwo akudziwa kuti Yesu adzathetsa kuipa konse pa dziko lapansi. Koma iwo akufuna kudziwa nthawi imene zimene’zi zidzachitika. Kodi ndi liti pamene Yesu adzadza kudzalamulira monga Mfumu?

Yesu akudziwa kuti otsatira ake pa dziko lapansi sadzakhala okhoza kumuona’nso. Izi ziri chifukwa chakuti iye adzakhala ali kumwamba, ndipo iwo sadzakhoza kumuona kumene’ko. Chotero Yesu akuuza atumwi ake zina za zinthu zimene zidzakhala zikuchitika pa dziko lapansi pamene iye akulamulira monga Mfumu kumwamba. Kodi ndi ziti zimene ziri zina za zinthu zimene’zi?

Yesu akunena kuti kudzakhala nkhondo zazikulu, anthu ambiri adzakhala akudwala, ndi anjala, upandu udzakhala woipa kwambiri, ndipo padzakhala zibvomezi zazikulu. Yesu ananena’nso kuti mbiri yabwino yonena za ufumu wa Mulungu idzalalikidwa kuli konse pa dziko lapansi. Kodi taona zinthu’zi zikuchitika m’nthawi yathu? Inde! Ndipo chotero tingathe kukhala otsimikizira kuti Yesu tsopano akulamulira kumwamba. Posachedwa iye adzathetsa kuipa konse pa dziko lapansi.