Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 11

Utawaleza Woyamba

Utawaleza Woyamba

KODI mukudziwa chinthu choyamba chimene Nowa anachita pamene iye ndi banja lake anatuluka m’chingalawa? Anapereka nsembe kwa Mulungu. Mungamuone akuchita izi m’chithunzi’chi pansi’pa, Nowa anapereka nsembe ya nyama’yi kuthokoza Mulungu kaamba ka kupulumutsa banja lake ku chigumula chachikulu.

Kodi muganiza kuti Yehova anakondwera ndi nsembe’yo? Inde. Chotero analonjeza Nowa kuti sakaononga’nso dziko lapansi ndi chigumula.

Posapita nthawi mtunda wonse unauma, ndipo Nowa ndi banja lake anayamba moyo watsopano kunja kwa chingalawa. Mulungu anawadalitsa nawauza kuti: ‘Balani ana ochuluka. Chulukani mpaka anthu atakhala pa dziko lonse lapansi.’

Koma pambuyo pake, anthu akadzamva za chigumula chachikulu, akaopa kuti chigumula chonga chimene’cho chingadzachitike’nso. Chotero Mulungu anapereka kanthu kena kokumbutsa anthu za lonjezo lake la kusadzetsa’nso chigumula pa dziko lonse. Kodi mudziwa chimene anapereka kuwakumbutsa. Chinali utawaleza.

Utawaleza umaoneka kumwamba itakata mvula pamene dzuwa liomba Mauta-aleza angakhale ndi maonekedwe ambiri okongola. Kodi munaonapo umodzi? Kodi mukuona uwo uli pa chithunzi’wo?

Nazi zimene Mulungu ananena: ‘Ndikulonjeza kuti anthu onse ndi zinyama sizidzaonongedwa’nso ndi chigumula. Ndikuika utawaleza wanga m’mitambo. Ndipo poonekera utawaleza, ndi dzauona ndi kukumbikira lonjezo langa’li.’

Chotero pamene muona utawaleza, kodi uyenera kukukumbutsaninji? Inde, lonjezo la Mulungu lakuti sadzaononga’nso dziko ndi chigumula chachikulu.