Mtima Wodikira Umatithandiza Kuti Tipirire
Kodi n’chiyani chinathandiza kuti Yeremiya apirire ngakhale kuti anakumana ndi mavuto aakulu?
-
Iye ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ‘adzaweramira’ anthu ake omwe analapa n’kuwapulumutsa m’mavuto awo
-
Iye anaphunzira ‘kunyamula goli lake ali mnyamata.’ Munthu akamapirira mayesero ali wamng’ono zimamuthandiza kuti adzathe kupirira mavuto omwe angadzakumane nawo m’tsogolo