Ndinayamba Kuona Magazi Mmene Mulungu Amawaonera
Ndinayamba Kuona Magazi Mmene Mulungu Amawaonera
Zimene Dokotola Wina Anafotokoza
NDINALI muholo yapachipatala chathu ndipo ndinkafotokozera madokotala anzanga zomwe tinapeza pambuyo poyeza mtembo wa munthu yemwe anali ndi chotupa chachikulu. Ndinauza anzangawo kuti: “Tapeza kuti munthuyu anamwalira chifukwa choti anaikidwa magazi, zomwe zinachititsa kuti maselo ofiira a magazi awonongeke komanso kuti impso yake isiye kugwira ntchito.”
Pulofesa wina anaimirira n’kulankhula molusa kuti, “Ukutanthauza kuti magazi omwe tinamuikawo anali olakwika?” Ndinamuyankha kuti, “Ayi si zimene ndikutanthauza.” Kenako ndinayamba kuwasonyeza zithunzi za tizigawo ta impso ya womwalirayo n’kuwauza kuti, “Mukhoza kuona mmene zikuonekera pachithunzichi kuti maselo ofiira awonongeka kwambiri ndipo tinganene kuti zimenezi n’zomwe zinachititsa kuti impso yake isiye kugwira ntchito.” * Aliyense muholomo anakwiya moti ndinangoti kakasi kusowa chonena. Ngakhale kuti ndinali nditangoyamba kumene udokotala pomwe iyeyo anali pulofesa, ndinkaona kuti zomwe ndinkanenazo zinali zoona.
Pamene zimenezi zinkachitika, ndinali ndisanakhale wa Mboni za Yehova. Ndinabadwa mu 1943 mumzinda wa Sendai, womwe uli kumpoto kwa dziko la Japan. Popeza kuti bambo anga anali katswiri woona za matenda osiyanasiyana ndiponso dokotala wa matenda a maganizo, nanenso ndinasankha kuphunzira zaudokotala. Mu 1970, ndinakwatirana ndi mtsikana wina dzina lake Masuko. Apa n’kuti ndili chaka chachiwiri kusukulu ya zaudokotala.
Kukhala Katswiri Woona za Matenda Osiyanasiyana
Pa nthawi imene ndinkapitiriza sukulu, Masuko ankagwira ntchito kuti tizipeza zinthu zofunika pa moyo. Maphunziro azaudokotala ankandisangalatsa kwambiri. Ndinkadabwa kwambiri kuona mmene thupi la munthu linapangidwira. Komabe, sindinkaganiza kuti pali Mlengi amene analilenga modabwitsa chonchi. Ndinkaganiza kuti kuchita kafukufuku wokhudzana ndi zachipatala kungandithandize kuti ndikhale ndi moyo waphindu. Choncho nditakhala dokotala ndinapitiriza maphunziro kuti ndikhale katswiri woona za matenda osiyanasiyana.
Pamene ndinkayeza matupi a anthu omwe anamwalira ndi khansa, ndinayamba kukaikira zoti kuika wodwala magazi n’kothandizadi. Odwala amene khansa yawo yafalikira kwambiri, amatha kukhala ndi vuto la kuchepa kwa magazi. Nthawi zambiri madokotala amanena kuti odwala apatsidwe magazi akamalandira chithandizo chomwe chimapha maselo a khansa, chifukwa chakuti chithandizochi chimachititsa kuti magazi achepe. Komabe, ndinayamba kuona kuti mwina kuika odwala magazi n’kumene kumachititsa kuti khansa ifalikire. Masiku ano ambiri amadziwa kuti kuika odwala magazi kumachititsa kuti chitetezo cha m’thupi chichepe. Zimenezi zingachititse kuti ngati anali ndi chotupa chiyambirenso ndipo moyo wa wodwalayo ungakhale pachiopsezo. *
Nkhani yomwe ndinakufotokozerani kumayambiriro ija inachitika mu 1975. Pulofesa ndinamutchula uja ndi katswiri woona za magazi ndipo ndi amene anaika munthu womwalirayo magazi. N’chifukwa chake anakwiya kwambiri atamva ndikunena kuti munthuyo wamwalira chifukwa choti anaikidwa magazi. Komabe ndinapitiriza kufotokoza zimene ndinkanena ndipo pang’onopang’ono mtima wake unakhala m’malo.
Sikudzakhalanso Matenda Kapena Imfa
Ndi pa nthawi imeneyi pamene mayi wina wachikulire, yemwe anali wa Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu kudzacheza ndi mkazi wanga. Pamene ankacheza naye, mayiyo anatchula dzina lakuti “Yehova” ndipo mkazi wanga anamufunsa kuti limatanthauza chiyani. Mayiyo anayankha kuti, “Yehova ndi dzina la Mulungu woona.” Masuko ankawerenga Baibulo kuyambira ali mwana koma m’Baibulo lakelo dzina la Mulungu linachotsedwamo ndipo m’malomwake anaikamo dzina lakuti “AMBUYE.” Pamenepo anazindikira kuti Mulungu ali ndi dzina.
Nthawi yomweyo Masuko anayamba kuphunzira Baibulo ndi mayi wa Mboniyo. Nditaweruka kuntchito, ndinakafika kunyumba cha m’ma 1 koloko usiku ndipo mkazi wanga anandiuza kuti, “Baibulo limanena kuti matenda ndi imfa zidzathatu.” Ndinamuyankha kuti, “Zitatero zingakhale zosangalatsa.” Iye ananenanso kuti, “Ndiye popeza dziko latsopano layandikira, sindikufuna kuti muzingotaya nthawi yanu.” Nditamva zimenezi ndinaganiza kuti akufuna ndisiye ntchito yanga yaudokotala, choncho ndinakwiya kwambiri moti zinthu zinasokonekera.
Komabe, mkazi wanga sanasiye kundifotokozera mfundo za m’Baibulo. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kupeza malemba amene angandifike pamtima ndipo anandionetsa. Lemba lomwe linandifika pamtima kwambiri ndi la Mlaliki 2:22, 23. Lembali limati: “Pakuti munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene waigwira mwakhama, ndiponso imene wasautsika nayo mtima poigwira padziko lapansi pano? . . . Usiku mtima wake sugona. Izinso n’zachabechabe.” Zimenezi ndi zimene ineyo ndinkachita. Ndinkangokhalira kugwira ntchito ndipo sindinkasangalala.
Lamlungu lina m’mawa mu July 1975, mkazi wanga ananyamuka n’kupita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Pa tsikuli nanenso ndinaganiza zoti ndipiteko. Mkazi wanga atandiona anadabwa kwambiri ndipo a Mboni anandilandira mwansangala kwambiri. Kungoyambira nthawi imeneyo, sindinkaphonya misonkhano yonse ya Lamlungu. Patapita mwezi umodzi, wa Mboni wina anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Kenako mkazi wanga anabatizidwa patapita miyezi itatu kuchokera pamene a Mboni anayamba kumuyendera.
Ndinagwirizana Ndi Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Magazi
Posakhalitsa ndinaphunzira m’Baibulo kuti Akhristu ayenera kupewa magazi. (Machitidwe 15:28, 29; Genesis 9:4) Popeza ndinkakaikira kale kuti kuika wodwala magazi ndi kothandiza, sindinavutike kugwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya magazi. * Ndinkadziuza kuti, ‘Ngati kuli Mlengi ndipo amanena zimenezo, ndiye kuti ndi zolondola.’
Ndinaphunziranso kuti anthu amadwala ndiponso kufa chifukwa chakuti anatengera uchimo wa Adamu. (Aroma 5:12) Pa nthawiyi n’kuti ndikupanga kafukufuku wokhudza matenda amitsempha ya magazi. Anthufe tikamakalamba, mitsempha imayamba kuchepa komanso kulimba zomwe zimachititsa kuti munthu akhale ndi mavuto monga matenda a mtima, kuphulika kwa mitsempha ya muubongo komanso matenda a impso. Choncho, n’zomveka kunena kuti zimenezi zimachitika chifukwa cha uchimo womwe tinatengera kwa Adamu. Nditangophunzira zimenezi, chidwi changa pa nkhani zachipatala chinayamba kuchepa. Ndi Yehova yekha amene adzathetse matenda ndi imfa.
Mu March 1976, ndinasiya maphunziro azachipatala omwe ndinkachita kuyunivesite. Apa n’kuti patadutsa miyezi 7 kuchokera pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo. Ndinkaopa kuti sindingadzagwirenso ntchito yaudokotala, komabe ndinadzapeza ntchito pachipatala china. Kenako mu May 1976, ndinabatizidwa. Ndinaganiza kuti njira yabwino kwambiri yomwe ndingagwiritse ntchito moyo wanga ndi kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse kapena kuti kuchita upainiya. Choncho mu July 1977, ndinayamba upainiya.
Ndinafotokoza Mmene Mulungu Amaonera Magazi
Mu November 1979, ine ndi Masuko tinasamukira mumpingo wina wa m’Boma la Chiba, womwe unkafunika olalikira ambiri. Ndinapeza ntchito kuchipatala china komwe ndinkagwirako masiku ochepa. Pa tsiku loyamba madokotala ochita opaleshoni anandizungulira. Iwo ankangondifunsa kuti: “Monga wa Mboni za Yehova, kodi ungatani ngati kwabwera wodwala yemwe akufunika kuikidwa magazi?”
Ndinawayankha mwaulemu kuti ndingatsatire zimene Mulungu amanena pa nkhani ya magazi. Ndinawafotokozera kuti pali njira zina zothandizira odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi ndiponso kuti ndidzayesetsa kuchita zomwe ndingathe kuti ndipereke thandizo loyenerera kwa odwala. Titakambirana kwa pafupifupi ola limodzi, mkulu wa madokotala ochita maopaleshoni anayankha kuti, “Ineyo ndamvetsa. Koma ngati kwabwera wodwala amene wataya magazi ambiri, ifeyo tidzamuthandiza.” Anthu ambiri ankamuopa mkuluyu chifukwa anali wovuta koma pambuyo pa kukambiranaku, tinayamba kugwirizana ndipo nthawi zonse ankalemekeza zimene ndimakhulupirira.
Sitinagonje Titayesedwa pa Nkhani ya Magazi
Pamene tinkatumikira ku Chiba, likulu la Mboni za Yehova linali likumangidwa mumzinda wa Ebina. Chifukwa choti ndinali dokotala, ine ndi mkazi wanga tinkapita kumeneko kamodzi pa mlungu, kukathandiza a Mboni ongodzipereka omwe ankamanga maofesi atsopano otchedwa Beteli. Patatha miyezi yochepa, tinaitanidwa kuti tizikatumikira nthawi zonse pa Beteli ya ku Ebina. Choncho mu March 1981, tinayamba kukhala m’nyumba zongoyembekezera zomwe munkakhala antchito ongodzipereka oposa 500. Kum’mawa ndinkathandiza kukonza mabafa ndi matoileti ndipo masana ndinkagwira ntchito zachipatala.
Mmodzi mwa anthu amene ndinkawathandiza anali Mlongo Ilma Iszlaub, yemwe anachokera ku Australia mu 1949 kudzachita umishonale ku Japan. Mlongoyu anali ndi khansa ya m’magazi ndipo madokotala ake anamuuza kuti wangotsala ndi miyezi yochepa kuti amwalire. Iye anakana kulandira magazi ndipo anasankha kukhala pa Beteli kwa masiku otsala a moyo wake. Pa nthawiyo kunalibe mankhwala monga erythropoietin, omwe amathandiza kuti thupi la munthu lizipanga magazi ochuluka. Nthawi zina magazi ake ankatsika kwambiri kufika pa magalamu atatu kapena 4 (magazi a munthu wabwinobwino amakhala magalamu 12 mpaka 15). Komabe ndinayesetsa kumuthandiza mmene ndingathere. Mlongo Ilma anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mpaka pamene anamwalira mu January 1988, pambuyo pa zaka 7.
Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova ongodzipereka omwe amagwira ntchito pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Japan, akhala akuchitidwa maopaleshoni. N’zosangalatsa kwambiri kuti madokotala am’zipatala zapafupi akhala akuchita maopaleshoni amenewa popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ndakhala ndikuitanidwa kuti ndikaonerere akamachita maopaleshoniwa ndipo nthawi zina ndinkathandiza nawo. Ndimayamikira kwambiri madokotala amene amalemekeza zimene a Mboni za Yehova amasankha pa nkhani ya magazi. Kugwira nawo ntchito limodzi kwandipatsa mwayi wowauza zimene ndimakhulupirira. Posachedwapa mmodzi wa madokotalawa wabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.
N’zochititsa chidwi kuti zimene madokotala akhala akuchita pothandiza a Mboni za Yehova popanda kugwiritsa ntchito magazi, zathandiza kuti madokotala atulukire njira zina zabwino kwambiri zothandizira odwala. Kuchita maopaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi kwathandiza anthu kudziwa ubwino wopewa kuika odwala magazi. Kafukufuku akusonyeza kuti odwala amene achitidwa opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi, amachira mwamsanga komanso sakhala ndi mavuto ambiri.
Ndikupitiriza Kuphunzira kwa Dokotala Wamkulu
Ndikupitiriza kuphunzira zinthu zatsopano zachipatala. Komabe, sindinasiye kuphunzira kuchokera kwa Yehova yemwe ndi dokotala wamkulu. Iye samangoona maonekedwe athu koma amatidziwa bwino kwambiri. (1 Samueli 16:7) Monga dokotala, ndikamathandiza wodwala aliyense, ndimayesetsa kuganizira mmene akumvera m’malo momangoona matenda ake. Zimenezi zimandichititsa kuti ndimuthandize bwino kwambiri.
Panopa ndikupitiriza kutumikira pa Beteli. Chinthu chimene chimandisangalatsa kwambiri ndi kuthandiza anthu kudziwa zokhudza Yehova kuphatikizapo mmene iye amaonera magazi. Ndikuyembekezera kuti posachedwapa Yehova Mulungu, yemwe ndi Dokotala Wamkulu, adzachotsa matenda onse komanso imfa.—Yofotokozedwa ndi Yasushi Aizawa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Mogwirizana ndi zimene buku lina lolembedwa ndi Dr. Denise M. Harmening limanena, “n’kupita kwa nthawi maselo ofiira a magazi akhoza kuyamba kuwonongeka kuchokera pamene munthu wapatsidwa magazi.” Zimenezi zimachitika “ngati munthu anaikidwa magazi, anali woyembekezera kapenanso ngati anaikidwa ziwalo zina ziwalo zake zitasiya kugwira ntchito.” Kwa odwala oterewa, asilikali am’thupi omwe amachititsa kuti thupi lawo liyambe kuwononga magazi omwe awaikawo, “saonekera madokotala akamawayeza.” (Modern Blood Banking and Transfusion Practices) Mogwirizana ndi buku lakuti Dailey’s Notes on Blood, “magazi a munthu akhoza kuwonongeka ngakhale ataikidwa magazi ochepa kwambiri omwe sakugwirizana ndi thupi la wodwala. Impso ikasiya kugwira ntchito imalephera kuchotsa zoipa m’thupi lake, choncho pang’ono ndi pang’ono zimatha kuyambitsa vuto lalikulu.”
^ ndime 8 Buku lina linati: Odwala khansa ambiri amamwalira msanga akakhala kuti apatsidwa magazi opaleshoni isanachitike kapena pambuyo pake, kusiyana ndi amene sanapatsidwe magazi.—Journal of Clinical Oncology, August 1988.
^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya magazi, onani kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? Kabukuka n’kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
“Ndinawafotokozera kuti pali njira zina zothandizira odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi ndiponso kuti ndidzayesetsa kuchita zomwe ndingathe kuti ndipereke thandizo loyenerera kwa odwala”
[Mawu Otsindika patsamba 15]
“Kuchita maopaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi kwathandiza anthu kudziwa ubwino wopewa kuika odwala magazi”
[Chithunzi patsamba 15]
Pamwamba: Ndikukamba nkhani ya m’Baibulo
Kumanja: Panopa, ndili ndi mkazi wanga Masuko